Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.
Yohane 13:11 - Buku Lopatulika Pakuti anadziwa amene adzampereka Iye; chifukwa cha ichi anati, Simuli oyera nonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti anadziwa amene adzampereka Iye; chifukwa cha ichi anati, Simuli oyera nonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu ankamudziŵa munthu wodzampereka kwa adani ake, nchifukwa chake adaati, “Si nonsenu muli oyera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti Iye anadziwa amene adzamupereka, ndipo nʼchifukwa chake anati saliyense wa inu ali woyera. |
Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.
Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,
Yesu m'mene adanena izi, anavutika mumzimu, nachita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine.
Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa. Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote.
Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.
ndipo sanasowe wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.