Yohane 13:10 - Buku Lopatulika Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adamuuza kuti, “Munthu amene wasamba, wayera yense. Palibe chifukwa choti asambenso, koma kungosamba mapazi okha basi. Tsono inu mwayera, koma osati nonsenu ai.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Munthu amene wasamba amangofunika kusamba mapazi ake okha chifukwa thupi lake lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, ngakhale kuti si aliyense mwa inu.” |
Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israele zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zochimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati chotsala.
Ndipo iye amene anachotsa mbuzi ipite kwa Azazele atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, ndipo atatero alowenso kuchigono.
Ndi iye amene anazitentha atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, ndipo atatero alowenso kuchigono.
Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake.
Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.
Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.
Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.
Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.
Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.