Ndinamtsegulira bwenzi langalo; koma ndinampeza, bwenzi langa atachoka. Moyo wanga unalefuka polankhula iye: Ndinamfunafuna, osampeza; ndinamuitana, koma sanandivomere.
Yohane 12:8 - Buku Lopatulika Pakuti osauka muli nao pamodzi ndi inu nthawi zonse; koma simuli ndi Ine nthawi zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti osauka muli nao pamodzi ndi Ine nthawi zonse; koma simuli ndi Inu nthawi zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pajatu osauka muli nawo nthaŵi zonse, koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mudzakhala ndi osauka nthawi zonse, koma simudzakhala nane nthawi zonse.” |
Ndinamtsegulira bwenzi langalo; koma ndinampeza, bwenzi langa atachoka. Moyo wanga unalefuka polankhula iye: Ndinamfunafuna, osampeza; ndinamuitana, koma sanandivomere.
Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.
Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.
Tiana, katsala kanthawi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndinkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano.
Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.
Popeza waumphawi salekana m'dziko, chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.