Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Yohane 12:7 - Buku Lopatulika Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anachisungira ichi tsiku la kuikidwa kwanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anachisungira ichi tsiku la kuikidwa kwanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Mlekeni, mafutaŵa aŵasungire tsiku lodzaika maliro anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Mulekeni. Mafutawa anayenera kusungidwa mpaka tsiku loyika maliro anga. |
Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?
Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumvutiranji mkaziyu? Popeza andichitira Ine ntchito yabwino.
Pakuti mkaziyo, m'mene anathira mafuta awa pathupi panga, wandichitiratu ichi pa kuikidwa kwanga.
Ndipo taonani, munthu dzina lake Yosefe, ndiye mkulu wa milandu, munthu wabwino ndi wolungama