Yohane 12:44 - Buku Lopatulika Koma Yesu anafuula nati, Iye wokhulupirira Ine, sakhulupirira Ine, koma Iye wondituma Ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yesu anafuula nati, Iye wokhulupirira Ine, sakhulupirira Ine, koma Iye wondituma Ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adanena mokweza mau kuti, “Munthu wondikhulupirira, sakhulupirira Ine ndekha ai, koma amakhulupiriranso Iye amene adandituma. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yesu anafuwula nati, “Munthu aliyense amene akhulupirira Ine, sakhulupirira Ine ndekha, komanso Iye amene anandituma Ine. |
Iye wakulandira inu, andilandira Ine, ndi wakundilandira Ine, amlandira Iye amene ananditumiza Ine.
Munthu aliyense adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.
Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira aliyense amene ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine.
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo.
Pamenepo Yesu anafuula mu Kachisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndichokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.
chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.