Yohane 12:3 - Buku Lopatulika Pamenepo Maria m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Maria m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Maria adatenga mafuta onunkhira zedi a narido weniweni, amtengowapatali, okwanira theka la lita, nayamba kudzoza mapazi a Yesu, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake. M'nyumba monsemo mumvekere guu ndi fungo la mafutawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Mariya anatenga botolo la mafuta a nadi, onunkhira bwino kwambiri, amtengowapatali; Iye anadzoza mapazi a Yesu napukuta ndi tsitsi lake. Ndipo nyumba yonse inadzaza ndi fungo lonunkhira bwino la mafutawo. |
Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda.
Ha, chikondi chako nchokongola, mlongo wanga, mkwatibwi! Kodi chikondi chako sichiposa vinyo? Kununkhira kwa mphoka yako ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundumitundu!
koma chisoweka chinthu chimodzi, pakuti Maria anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.
Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino.
Koma ndiye Maria uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, amene mlongo wake Lazaro anadwala.
Ndipo m'mene anati ichi anachoka naitana Maria mbale wake m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe.
Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira.
Koma anadzanso Nikodemo, amene anadza kwa Iye usiku poyamba paja, alikutenga chisakanizo cha mure ndi aloe, monga miyeso zana.