Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwe, ndi mtundu umene sunakudziwe udzakuthamangira, chifukwa cha Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele; pakuti Iye wakukometsa.
Yohane 12:23 - Buku Lopatulika Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa Munthu alemekezedwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa Munthu alemekezedwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Yafika nthaŵi yoti Mwana wa Munthu alandire ulemerero wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Nthawi yafika yakuti Mwana wa Munthu alemekezedwe. |
Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwe, ndi mtundu umene sunakudziwe udzakuthamangira, chifukwa cha Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele; pakuti Iye wakukometsa.
Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisisi kutenga ana ako aamuna kutali, golide wao ndi siliva wao pamodzi nao, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele, popeza Iye wakukometsa iwe.
Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake:
Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a ochimwa.
Ndipo Iye anapita m'tsogolo pang'ono, nagwa pansi, napemphera kuti ngati nkutheka nthawi imene impitirire.
Ndipo anadza kachitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; chakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a anthu ochimwa.
Izi sanazidziwe ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi.
Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi.
Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro.
Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo.