Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.
Yohane 12:12 - Buku Lopatulika M'mawa mwake khamu lalikulu la anthu amene adadza kuchikondwerero, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'mawa mwake khamu lalikulu la anthu amene adadza kuchikondwerero, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'maŵa mwake anthu ambirimbiri amene anali atabwera ku chikondwerero cha Paska chija, adamva kuti Yesu akubwera ku Yerusalemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku lotsatira, gulu lalikulu la anthu lomwe linabwera kuphwando linamva kuti Yesu anali mʼnjira kupita ku Yerusalemu. |
Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.
Chifukwa cha ichinso khamulo linadza kudzakomana ndi Iye, chifukwa anamva kuti Iye adachita chizindikiro ichi.
Pamenepo khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti ali pomwepo; ndipo anadza, si chifukwa cha Yesu yekha, koma kuti adzaone Lazaro, amene adamuukitsa kwa akufa.