Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.
Yohane 12:11 - Buku Lopatulika pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pakuti chifukwa cha iyeyo anthu ambiri ankaŵachokera nkumakhulupirira Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero pakuti chifukwa cha iye Ayuda ambiri amapita kwa Yesu ndi kumukhulupirira. |
Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.
Chifukwa chake ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Maria, m'mene anaona chimene anachita, anakhulupirira Iye.
Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.
Chifukwa cha ichinso khamulo linadza kudzakomana ndi Iye, chifukwa anamva kuti Iye adachita chizindikiro ichi.
Kungakhale kotero, ambiri a mwa akulu anakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze, kuti angaletsedwe m'sunagoge,
Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?
Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.