Yohane 11:9 - Buku Lopatulika Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Kodi suja usana uli ndi maora khumi ndi aŵiri? Munthu akayenda masana, sakhumudwa, chifukwa amaona kuŵala kwa dzikoku. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Kodi sipali maora khumi ndi awiri pa tsiku? Munthu amene amayenda masana sapunthwa, popeza akuona chifukwa cha kuwala kwa dziko lapansi. |
Adzadza ndi kulira, ndipo ndidzawatsogolera ndi mapembedzero, ndidzawayendetsa kumitsinje yamadzi, m'njira yoongoka m'mene sadzaphunthwa, pakuti ndili Atate wake wa Israele, ndipo Efuremu ali mwana wanga woyamba.
Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.
Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito.