Yohane 11:8 - Buku Lopatulika Ophunzira ananena ndi Iye, Rabi, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ophunzira ananena ndi Iye, Rabi, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ophunzira akewo adati, “Aphunzitsi, tsopano apa Ayuda ankafuna kukuponyani miyala, ndiye mukuti mupitenso komweko?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ophunzira akewo anati, “Rabi, posachedwa pomwepa Ayuda anafuna kukugendani ndi miyala, koma Inu mukupitanso komweko?” |
Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Maria, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.
Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.