Yohane 11:57 - Buku Lopatulika Koma ansembe aakulu ndi Afarisi adalamula kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, aulule, kuti akamgwire Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ansembe aakulu ndi Afarisi adalamula kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, aulule, kuti akamgwire Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma akulu a ansembe ndi Afarisi anali atalamula kuti aliyense akadziŵa kumene kuli Yesu, aŵadziŵitse, kuti akamgwire. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma akulu a ansembe ndi Afarisi anapereka lamulo kuti ngati wina aliyense adziwe kumene kunali Yesu, iye akawawuze kuti akamugwire. |
Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.
Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge.