Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali nao osenga nkhosa zake ku Baala-Hazori pafupi pa Efuremu; ndipo Abisalomu anaitana ana aamuna onse a mfumu.
Yohane 11:54 - Buku Lopatulika Chifukwa chake Yesu sanayendeyendenso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake Yesu sanayandeyendanso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake Yesu sankayenda poyera pakati pa anthu. Koma adachokako napita ku dziko limene linali pafupi ndi chipululu, ku mudzi wina dzina lake Efuremu, ndipo adakhala kumeneko pamodzi ndi ophunzira ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chifukwa cha ichi Yesu sanayendenso moonekera pakati pa Ayuda. Mʼmalo mwake Iye anapita ku chigawo cha kufupi ndi chipululu, ku mudzi wa Efereimu, kumene Iye anakhalako ndi ophunzira ake. |
Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali nao osenga nkhosa zake ku Baala-Hazori pafupi pa Efuremu; ndipo Abisalomu anaitana ana aamuna onse a mfumu.
Ndipo Abiya analondola Yerobowamu, namlanda mizinda yake, Betele ndi midzi yake, ndi Yesana ndi midzi yake, ndi Efuroni ndi midzi yake.
Ndipo anachoka kunkanso tsidya lija la Yordani, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko.
Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi mu Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhule kanthu.
Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda mu Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.
Koma pamene abale ake adakwera kunka kuchikondwerero, pomwepo Iyenso anakwera, si poonekera, koma monga mobisalika.
Pakuti palibe munthu achita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera. Ngati muchita izi, dzionetsereni eni nokha kwa dziko lapansi.