Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe.
Yohane 11:53 - Buku Lopatulika Chifukwa chake, kuyambira tsiku lomwelo anapangana kuti amuphe Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake, kuyambira tsiku lomwelo anapangana kuti amuphe Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kuyambira tsiku limenelo akulu aja a Ayuda adayamba kupangana zoti amuphe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho kuyambira tsiku limeneli iwo anakonzekera za kuti amuphe. |
Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe.
Koma ndinawachitira umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? Mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikenso pa Sabata.
Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira ntchito, ndi gawo lina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi malaya achitsulo; ndi akulu anali m'mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda.
Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,
Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.
Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Ndikakufotokozerani, kodi simudzandipha ine? Ndipo ndikakupangirani, simudzandimvera ine.
Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mzinda muno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.
Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.
Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;
Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:
Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.
Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda mu Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.