Yohane 11:44 - Buku Lopatulika Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pomwepo munthu amene adaamwalirayo adatuluka, miyendo yake ndi manja ake zili zomangidwa ndi nsalu zamaliro. Nkhope yake inali yokutidwa ndi nsalu. Yesu adaŵauza kuti, “Mmasuleni, ndipo mlekeni azipita.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Munthu womwalirayo anatuluka, womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za ku manda, ndi nkhope yake yokulungidwa nsalu. Yesu anawawuza kuti, “Mʼmasuleni, ndipo muloleni apite.” |
Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.
Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ichi munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya.
Yesu ananena, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, ananena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai.
Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.
ndi mlezo, umene unali pamutu pake, wosakhala pamodzi ndi nsalu zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena.
Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna.
Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.
amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.
ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa.