Ndipo iwo anachita mantha aakulu, nanenana wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
Yohane 11:43 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene adanena izi, anafuula ndi mau aakulu, Lazaro, tuluka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene adanena izi, anafuula ndi mau akulu, Lazaro, tuluka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atatero adaitana mokweza mau kuti, “Lazaro, tuluka!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, “Lazaro, tuluka!” |
Ndipo iwo anachita mantha aakulu, nanenana wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.
Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke.
Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.
Pamenepo khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti ali pomwepo; ndipo anadza, si chifukwa cha Yesu yekha, koma kuti adzaone Lazaro, amene adamuukitsa kwa akufa.
Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?
Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.
Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu akuchiritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo.
Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga.