Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye.
Yohane 11:34 - Buku Lopatulika nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi Iye, Ambuye, tiyeni mukaone. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi Iye, Ambuye, tiyeni mukaone. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adaŵafunsa kuti, “Mudamuika kuti?” Iwo adati, “Ambuye, tiyeni mukaone.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anafunsa kuti, “Kodi mwamuyika kuti?” Iwo anayankha kuti, “Ambuye tiyeni mukaone.” |
Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye.
Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapachikidwa; anauka; sali pano; taonani, mbuto m'mene anaikamo Iye!
Nanena nao, Tiyeni, mukaone. Pamenepo anadza naona kumene anakhala; nakhala ndi Iye tsiku lomwelo; panali monga ora lakhumi.
Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini,
Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anachotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika Iye.