ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo.
Yohane 11:32 - Buku Lopatulika Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Maria atafika pamene panali Yesu, namuwona, adadzigwetsa kumapazi kwake nati, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mariya anafika pamalo pamene panali Yesu ndipo atamuona, anagwa pa mapazi ake ndipo anati, “Ambuye mukanakhala muli kuno mlongo wanga sakanamwalira.” |
ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo.
Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.
Ndipo onani, panadza munthu dzina lake Yairo, ndipo iye ndiye mkulu wa sunagoge; ndipo anagwa pamapazi ake a Yesu, nampempha Iye adze kunyumba kwake;
Koma ndiye Maria uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, amene mlongo wake Lazaro anadwala.
Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sakanatha kodi kuchita kuti asafe ameneyunso?
Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo.
Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima.