Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale cholowa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako.
Yohane 11:22 - Buku Lopatulika Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu zilizonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu zilizonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ngakhale tsopano, ndikudziŵa kuti Mulungu adzakupatsani zilizonse mungampemphe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ine ndikudziwa kuti ngakhale tsopano Mulungu adzakupatsani chilichonse chimene mudzamupempha.” |
Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale cholowa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako.
Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.
monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi lililonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha.
Tidziwa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo.