Yohane 11:18 - Buku Lopatulika Koma Betaniya anali pafupi pa Yerusalemu, nthawi yake yonga ya mastadiya khumi ndi asanu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Betaniya anali pafupi pa Yerusalemu, nthawi yake yonga ya mastadiya khumi ndi asanu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ku Betaniya kunali kufupi ndi ku Yerusalemu, mtunda wokwanira pafupi makilomita atatu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mudzi wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pa mtunda wosachepera makilomita atatu, |
Ndipo taonani, awiri a mwa iwo analikupita tsiku lomwelo kumudzi dzina lake Emausi, wosiyana ndi Yerusalemu mastadiya makumi asanu ndi limodzi.
Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Maria ndi mbale wake Marita.
Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anachita mantha.
Ndipo moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mzinda, ndipo mudatuluka mwazi moponderamo mphesa, kufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi.
Ndipo mzinda ukhala waphwamphwa; utali wake ulingana ndi kupingasa kwake: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wake, ndi kupingasa kwake, ndi kutalika kwake zilingana.