Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
Yohane 11:16 - Buku Lopatulika Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, adauza ophunzira anzake kuti, “Tiyeni ifenso tipite nao kuti tikafe naye pamodzi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, “Tiyeni nafenso tipite, kuti tikafere naye pamodzi.” |
Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
Petro ananena kwa Iye, Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iai. Anateronso ophunzira onse.
ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,
Ndipo ndikondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe Ine komweko, chakuti mukakhulupirire; koma tiyeni, tipite kwa iye.
Ophunzira ananena ndi Iye, Rabi, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi?
Petro ananena ndi Iye, Ambuye, sindingathe kukutsatani Inu tsopano chifukwa ninji? Ndidzataya moyo wanga chifukwa cha Inu.
Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimo, ndi Natanaele wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedeo, ndi awiri ena a ophunzira ake.
Ndipo pamene adalowa, anakwera kuchipinda chapamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andrea, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeo ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni Zelote, ndi Yudasi mwana wa Yakobo.