Yohane 11:14 - Buku Lopatulika Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu adaŵauza mosabisa kuti, “Lazaro wamwalira, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo kenaka anawawuza momveka kuti, “Lazaro wamwalira. |
Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiuzeni momveka.
Ndipo ndikondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe Ine komweko, chakuti mukakhulupirire; koma tiyeni, tipite kwa iye.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.
Ophunzira ake ananena, Onani, tsopano mulankhula zomveka, ndipo mulibe kunena chiphiphiritso.