Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Yohane 11:13 - Buku Lopatulika

Koma Yesu adanena za imfa yake; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma Yesu adanena za imfa yake; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Iwo ankayesa kuti akunena za tulo teniteni, koma Yesu ankanena za imfa yake ya Lazaro.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesu ankayankhula za imfa yake koma ophunzira ake ankaganiza kuti amanena za tulo chabe.

Onani mutuwo



Yohane 11:13
5 Mawu Ofanana  

ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafe koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete.


Ndipo anthu onse analikumlira iye ndi kudziguguda pachifuwa. Koma Iye anati, Musalire; pakuti iye sanafe, koma wagona tulo.


Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.


Chifukwa chake ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, ngati ali m'tulo adzachira.


Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira.