Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo.
Yohane 11:11 - Buku Lopatulika Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atatero adaŵauza kuti, “Lazaro, bwenzi lathu, wagona tulo, koma ndipita kuti ndikamdzutse ku tulo taketo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye atatha kunena izi, anapitirira kuwawuza iwo kuti, “Bwenzi lathu Lazaro wagona tulo; koma Ine ndikupita kumeneko kukamudzutsa.” |
Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo.
Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pamaso pa ana anu Israele, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?
Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.
Koma iwe, Israele, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa;
Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha.
ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafe koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete.
Ndipo m'mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafe, koma ali m'tulo.
Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.
Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau aakulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo.
Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, nadzatsata ndi chigololo milungu yachilendo ya dziko limene analowa pakati pake, nadzanditaya Ine, ndi kuthyola chipangano changa ndinapangana naocho.
amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye.
ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.