Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga, inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.
Yohane 11:10 - Buku Lopatulika Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, chifukwa mulibe kuunika mwa iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, chifukwa mulibe kuunika mwa iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma akayenda usiku, amakhumudwa chifukwa kuŵalako alibe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma amene akuyenda usiku amapunthwa, chifukwa kuwalako alibe.” |
Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga, inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.
Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.
Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanaphunthwe pa mapiri achizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Iye asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii.
Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.
ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo chifukwa cha mau, iye akhumudwa pomwepo.
Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.
Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi.