Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye.
Yohane 11:1 - Buku Lopatulika Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Maria ndi mbale wake Marita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Maria ndi mbale wake Marita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Panali munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadwala. Anali wa ku mudzi wa Betaniya, kwao kwa Maria ndi mbale wake Marita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano munthu wina dzina lake Lazaro anadwala. Iye anali wa ku Betaniya, mudzi wa Mariya ndi mchemwali wake Marita. |
Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake aamuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye.
Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, paphiri la Azitona, anatuma awiri a ophunzira ake,
Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.
Koma Betaniya anali pafupi pa Yerusalemu, nthawi yake yonga ya mastadiya khumi ndi asanu;
koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Maria, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.
Pamenepo khamulo limene linali pamodzi ndi Iye, m'mene anaitana Lazaro kutuluka kumanda, namuukitsa kwa akufa, anachita umboni.
Pamenepo khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti ali pomwepo; ndipo anadza, si chifukwa cha Yesu yekha, koma kuti adzaone Lazaro, amene adamuukitsa kwa akufa.
Ndipo kunali m'masiku awa, kuti anadwala iye, namwalira; ndipo atamsambitsa iye anamgoneka m'chipinda chapamwamba.