nanena kwa anyamata ake, Uyo ndiye Yohane Mbatizi; anauka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye.
Yohane 10:41 - Buku Lopatulika Ndipo ambiri anadza kwa Iye; nanena kuti, Sanachita chizindikiro Yohane; koma zinthu zilizonse Yohane ananena za Iye zinali zoona. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ambiri anadza kwa Iye; nanena kuti, Sanachita chizindikiro Yohane; koma zinthu zilizonse Yohane ananena za Iye zinali zoona. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ambiri adadza kwa Iye, nkumanena kuti, “Yohane sadachite chizindikiro chozizwitsa ai, koma zonse zimene ankanena za Munthuyu zinali zoonadi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anthu ambiri anabwera kwa Iye. Iwo anati, “Ngakhale kuti Yohane sanachite chizindikiro chodabwitsa, zonse zimene Yohane ananena za munthu uyu zinali zoona.” |
nanena kwa anyamata ake, Uyo ndiye Yohane Mbatizi; anauka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye.
Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.
Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;
Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.