Yohane 10:40 - Buku Lopatulika Ndipo anachoka kunkanso tsidya lija la Yordani, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anachoka kunkanso tsidya lija la Yordani, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adabwereranso kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, kumene Yohane ankabatizira anthu poyamba paja, ndipo adakhala komweko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yesu anabwereranso kutsidya la mtsinje wa Yorodani kumalo kumene Yohane ankabatiza mʼmasiku akale. Iye anakhala kumeneko |
Chifukwa chake Yesu sanayendeyendenso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake.
Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye.
Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda mu Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye.