Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
Yohane 10:34 - Buku Lopatulika Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'chilamulo chanu, Ndinati Ine, Muli milungu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'chilamulo chanu, Ndinati Ine, Muli milungu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Kodi m'Malamulo mwanu suja mudalembedwa kuti ‘Mulungu adati, Ndinu milungu?’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anawayankha kuti, “Kodi sizinalembedwa mʼmalamulo anu kuti, ‘Ine ndanena kuti ndinu milungu?’ |
Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.
Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati m'kamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Taona, ndakuika ngati Mulungu kwa Farao; ndi Aroni mkulu wako adzakhala mneneri wako.
Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka),
Pamenepo khamulo linayankha Iye, Tidamva ife m'chilamulo kuti Khristu akhala kunthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa Munthu amene ndani?
Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.
Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.