Yohane 10:26 - Buku Lopatulika Koma inu simukhulupirira, chifukwa simuli a mwa nkhosa zanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma inu simukhulupirira, chifukwa simuli a mwa nkhosa zanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma inu simukhulupirira konse, chifukwa simuli a m'gulu la nkhosa zanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero koma inu simukhulupirira chifukwa simuli a gulu lankhosa zanga. |
Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja.
Ndipo ananena, Chifukwa cha ichi ndinati kwa inu, kuti palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate.
Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu.
Ife ndife ochokera mwa Mulungu; iye amene azindikira Mulungu atimvera; iye wosachokera mwa Mulungu satimvera ife. Momwemo tizindikira mzimu wa choonadi, ndi mzimu wa chisokeretso.