Ndipo Solomoni anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israele onse anapereka nyumbayo ya Yehova.
Yohane 10:22 - Buku Lopatulika Koma kunali phwando la kukonzetsanso mu Yerusalemu; nyengoyo ndi yachisanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma kunali phwando la kukonzetsanso m'Yerusalemu; nyengoyo ndi yachisanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kuperekedwanso kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nyengo yozizira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kupatulidwa kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nthawi yozizira, |
Ndipo Solomoni anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israele onse anapereka nyumbayo ya Yehova.
Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ya ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi makumi awiri. Momwemo mfumu ndi anthu onse anapereka nyumba ya Mulungu.
Ndipo ana a Israele, ansembe ndi Alevi, ndi ana otsala a ndende, anapereka nyumba iyi ya Mulungu mokondwera.
Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda.
Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa chiwanda. Kodi chiwanda chikhoza kumtsegulira maso wosaona?