Yohane 10:21 - Buku Lopatulika Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa chiwanda. Kodi chiwanda chikhoza kumtsegulira maso wosaona? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa chiwanda. Kodi chiwanda chikhoza kumtsegulira maso wosaona? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma ena ankati, “Mau ameneŵa si a munthu wogwidwa ndi mizimu yoipa. Kodi mizimu yoipa nkupenyetsa anthu akhungu?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ena anati, “Awa si mawu a munthu wogwidwa ndi ziwanda. Kodi ziwanda zingathe bwanji kutsekula maso a wosaona?” |
Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi?
Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.
Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Pamene ananena izi, analavula pansi, nakanda thope ndi malovuwo, napaka thopelo m'maso,