Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake?
Yohane 10:19 - Buku Lopatulika Panakhalanso kutsutsana pakati pa Ayuda chifukwa cha mau awa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Panakhalanso kutsutsana pakati pa Ayuda chifukwa cha mau awa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu adaayambanso kutsutsana okhaokha chifukwa cha mau ameneŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa mawu awa Ayuda anagawikananso. |
Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake?
Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.
Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndivomereza penapo.
pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?