Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.
Yohane 10:17 - Buku Lopatulika Chifukwa cha ichi Atate andikonda Ine, chifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa cha ichi Atate andikonda Ine, chifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Nchifukwa chake Atate amandikonda, popeza kuti ndikupereka moyo wanga kuti ndikautengenso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake Atate anga amandikonda, popeza Ine ndikupereka moyo wanga kuti ndiwutengenso. |
Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.
Chinakondweretsa Yehova chifukwa cha chilungamo chake kukuza chilamulo, ndi kuchilemekeza.
monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.
Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga.
Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa; mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani ndi mafuta a chikondwerero chenicheni koposa anzanu.
Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu aliyense.