Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
Yohane 1:49 - Buku Lopatulika Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Natanaele adati, “Aphunzitsi, ndinudi Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israele.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Natanieli ananena kuti, “Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu; Inu ndinu Mfumu ya Israeli.” |
Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.
Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.
Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.
atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza.
Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
Yehova wachotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israele, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso choipa.
Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
Ndipo iwo amene anali m'ngalawamo anamgwadira, nanena, Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.
nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.
Tauzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.
Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale.
Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero.
Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye mfumu ya Aisraele; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye.
Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate.
Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.
Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.
nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere mu Mwamba, ndi ulemerero mu Mwambamwamba.
Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa chifuwa cha Atate, Iyeyu anafotokozera.
Koma Yesu anacheuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna chiyani? Ndipo anati kwa Iye, Rabi (ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti?
Yesu anayankha nati kwa iye, Chifukwa ndinati kwa iwe kuti ndinakuona pansi pa mkuyu ukhulupirira kodi? Udzaona zoposa izi.
Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga.