Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.
Yohane 1:48 - Buku Lopatulika Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Natanaele adamufunsa kuti, “Mwandidziŵa bwanji?” Yesu adati, “Muja unakhala patsinde pa mkuyu paja, Filipo asanakuitane, Ine ndinakuwona.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Natanieli anafunsa kuti, “Kodi mwandidziwa bwanji?” Yesu anayankha kuti, “Ine ndinakuona iwe utakhala pansi pamtengo wamkuyu Filipo asanakuyitane.” |
Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva.
Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa mu Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu.
ndipo sanasowe wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.
Pamenepo Yesu, pokweza maso ake, ndi kuona kuti khamu lalikulu lilinkudza kwa Iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?
Filipo anayankha Iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono.
zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu.
Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.