Iwo amene sanafunse za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaire andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunatchule dzina langa.
Yohane 1:43 - Buku Lopatulika M'mawa mwake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, napeza Filipo. Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'mawa mwake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, napeza Filipo. Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'maŵa mwake Yesu adaganiza zopita ku Galileya. Adapeza Filipo, namuuza kuti, “Unditsate.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pa tsiku lotsatira Yesu anaganiza zopita ku Galileya. Atamupeza Filipo, anati kwa iye, “Nditsate.” |
Iwo amene sanafunse za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaire andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunatchule dzina langa.
Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
Ndipo Yesu popita, kuchokera kumeneko, anaona munthu, dzina lake Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.
M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!
Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa mu Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu.
Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita mu Kana wa mu Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye.
Pamenepo Yesu, pokweza maso ake, ndi kuona kuti khamu lalikulu lilinkudza kwa Iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa?
Filipo anayankha Iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono.
Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene anandigwirira Khristu Yesu.