Ndipo Isaki ananena ndi Abrahamu atate wake, nati, Atate wanga; ndipo iye anati, Ndine pano, mwana wanga. Ndipo anati, Taonani moto ndi nkhuni; koma mwanawankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?
Yohane 1:36 - Buku Lopatulika ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene adaona Yesu akuyenda, iye adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye ataona Yesu akudutsa anati, “Taonani Mwana Wankhosa wa Mulungu!” |
Ndipo Isaki ananena ndi Abrahamu atate wake, nati, Atate wanga; ndipo iye anati, Ndine pano, mwana wanga. Ndipo anati, Taonani moto ndi nkhuni; koma mwanawankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?
Yang'anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina.
M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!
Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.