Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Yohane 1:30 - Buku Lopatulika Ndiye amene ndinati za Iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiye amene ndinati za Iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyu ndi amene ndinkanena uja kuti, ‘Pambuyo panga pakubwera munthu wopambana ine, pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uyu ndi amene ndimatanthauza pamene ndinanena kuti, ‘Munthu amene akubwera pambuyo panga ndi wondiposa ine chifukwa analipo ine ndisanabadwe.’ |
Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula zingwe za nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Yohane achita umboni za Iye, nafuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za Iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; chifukwa anakhala woyamba wa ine.
Ndipo sindinamdziwe Iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israele, chifukwa cha ichi ndinadza ine kudzabatiza ndi madzi.
Ndipo ambiri anadza kwa Iye; nanena kuti, Sanachita chizindikiro Yohane; koma zinthu zilizonse Yohane ananena za Iye zinali zoona.