Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Yohane 1:26 - Buku Lopatulika Yohane anawayankha, nati, Ine ndibatiza ndi madzi; pakati pa inu paimirira amene simumdziwa, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yohane anawayankha, nati, Ine ndibatiza ndi madzi; pakati pa inu paimirira amene simumdziwa, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yohane adaŵayankha kuti, “Ine ndimabatiza ndi madzi, koma pakati panupa pali wina amene inu simukumdziŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yohane anayankha kuti, “Ine ndimabatiza ndi madzi, koma pakati panu payima amene simukumudziwa. |
Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula zingwe za nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Atate wolungama, dziko lapansi silinadziwe Inu, koma Ine ndinadziwa Inu; ndipo iwo anazindikira kuti munandituma Ine;
Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.
Chifukwa chake ananena ndi Iye, Ali kuti Atate wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukadadziwanso Atate wanga.
pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.
Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.
Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu.
Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.