Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.
Yohane 1:24 - Buku Lopatulika Ndipo otumidwawo anali a kwa Afarisi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo otumidwawo anali a kwa Afarisi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu aja adaaŵatuma ndi Afarisi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano Afarisi ena amene anatumidwa |
Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.
Ndipo pamene Iye anatuluka m'menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza Iye kolimba, ndi kumfunsa zinthu zambiri;
Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye.
Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.
Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?
Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi avomereza ponse pawiri.
andidziwa ine chiyambire, ngati afuna kuchitapo umboni, kuti ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa chipembedzero chathu.