Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.
Yohane 1:21 - Buku Lopatulika Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adamufunsanso kuti, “Nanga ndiwe yani? Ndiwe Eliya kodi?” Iye adati, “Iyai, sindine Eliya.” Iwo adati, “Kodi ndiwe Mneneri tikumuyembekeza uja?” Koma Yohane adayankha kuti, “Ainso.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anamufunsa kuti, “Nanga iwe ndiwe yani? Kodi ndiwe Eliya?” Iye anati, “Sindine.” “Kodi ndiwe Mneneri?” Iye anayankha kuti, “Ayi.” |
Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.
Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri.
Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.
Chifukwa chake anati kwa iye, Ndiwe yani? Kuti tibwezere mau kwa iwo anatituma ife. Unena chiyani za iwe wekha?
Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo?
Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi.