Chifukwa chake Ambuye ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israele, Ha! Ndidzatonthoza mtima wanga pochotsa ondivuta, ndi kubwezera chilango adani anga;
Yeremiya 9:9 - Buku Lopatulika Kodi sindidzawalanga chifukwa cha izi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi sindidzawalanga chifukwa cha izi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi zimenezi ndipanda kuŵalanga nazo? Monga ndisaulipsire mtundu wotere wa anthu?” Akutero Chauta Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi? akutero Yehova. ‘Kodi ndisawulipsire mtundu wotere wa anthu?’ ” |
Chifukwa chake Ambuye ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israele, Ha! Ndidzatonthoza mtima wanga pochotsa ondivuta, ndi kubwezera chilango adani anga;
Ndipo mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang'anira, ndi chipasuko chochokera kutali? Mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? Mudzasiya kuti ulemerero wanu?
Pakuti pa miyala yosalala ya m'chigwa pali gawo lako; iyo ndiyo gawo lako; ndiyo imene unaitsanulirira nsembe yothira, ndi kupereka nsembe yaufa. Kodi ndidzapembedzedwa pa zinthu zimenezi?
Apayesa bwinja; pandilirira ine, pokhala bwinja; dziko lonse lasanduka bwinja; chifukwa palibe munthu wosamalira.
Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.
Sindidzawalanga kodi chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?
Kodi sindidzawalanga chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu woterewu?
Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa.
Ndifuulira kwa Inu Yehova, pakuti moto wapsereza mabusa a m'chipululu, ndi malawi a moto anatentha mitengo yonse yakuthengo.