Yeremiya 7:5 - Buku Lopatulika Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi machitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi machitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu. Muzichitirana zolungama. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati mutasinthadi makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndi kumachitirana zolungama, |
Chitani uphungu, weruzani chiweruziro; yesa mthunzi wako monga usiku pakati pa usana; bisa opirikitsidwa, osawulula woyendayenda.
Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Chita chiweruzo m'mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m'dzanja la wosautsa, kungatuluke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, chifukwa cha ntchito zanu zoipa.
Kodi udzakhala mfumu, chifukwa iwe uyesa kuposa ena ndi mikungudza? Kodi atate wako sanadye ndi kumwa, ndi kuweruza molungama? Kumeneko kunamkomera.
Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano.
Chifukwa chake tsopano konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka choipa chimene ananenera inu.
Yehova wa makamu atero, Mulungu wa Israele, Konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndipo ndidzakukhalitsani inu m'malo ano.
naletsa dzanja lake pa wozunzika, wosalandira phindu kapena choonjezerapo, wochita maweruzo anga, nayenda m'malemba anga; uyu sadzafera mphulupulu ya atate wake, adzakhala ndi moyo ndithu.
wosapereka molira phindu, wosatenga choonjezerapo wobweza dzanja lake lisachite chosalungama, woweruza zoona pakati pa munthu ndi mnzake,
Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'mizinda mwake pozungulira pake, ndi m'dziko la kumwera, ndi m'chidikha munali anthu okhalamo?
Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-Giliyadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m'dziko la Kanani.