Yeremiya 6:4 - Buku Lopatulika Lalikirani nkhondo yakumenyana ndi iye; ukani, tikwere pakati pa usana. Tsoka kwa ife! Pakuti dzuwa lapendeka, mithunzi ya madzulo yatambasuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Lalikirani nkhondo yakumenyana ndi iye; ukani, tikwere pakati pa usana. Tsoka kwa ife! Pakuti dzuwa lapendeka, mithunzi ya madzulo yatambasuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adzanena kuti, “Konzekani kuti muuthire nkhondo mzindawu. Bwerani tiwuthire nkhondo masana ano.” “Koma tili ndi tsoka, dzuŵa lapendeka, zithunzithunzi zakumadzulo zikunka zitalika.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adzanena kuti, “Konzekani kuwuthira nkhondo mzindawo! Nyamukani, kuti tiwuthire nkhondo mzindawu masana ano. Koma tili ndi tsoka, dzuwa lapendeka, ndipo zithunzithunzi za kumadzulo zikunka zitalika. |
Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo pena mwana wa mbawala pa mapiri a mipata.
Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.
Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lake lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova.
Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova.
Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni.
Mulalikire ichi mwa amitundu, mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.
Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo.
Atero Yehova za aneneri akulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kufuula, Mtendere; ndipo aliyense wosapereka m'kamwa mwao, amkonzera nkhondo;
Pakuti Gaza adzasiyidwa, ndi Asikeloni adzakhala bwinja; adzaingitsa Asidodi usana, ndi Ekeroni adzazulidwa.