Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo.
Yeremiya 6:3 - Buku Lopatulika Abusa ndi nkhosa zao adzadza kwa iye; adzamanga mahema ao pomzinga iye; adzadya yense pokhala pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Abusa ndi nkhosa zao adzadza kwa iye; adzamanga mahema ao pomzinga iye; adzadya yense pokhala pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mafumu adzabwera ndi asilikali ao. Adzamanga zithando momzinga Yerusalemu, ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abusa ndi nkhosa zawo adzabwera kudzalimbana nawo; adzamanga matenti awo mowuzinga, ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.” |
Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo.
Abusa ambiri aononga munda wanga wampesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu.
Abusa ako aodzera, mfumu ya ku Asiriya; omveka ako apumula; anthu ako amwazika pamapiri, ndipo palibe wakuwasonkhanitsa.
Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo;