Yeremiya 51:4 - Buku Lopatulika Ndipo adzagwa ophedwa m'dziko la Ababiloni, opyozedwa m'miseu yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo adzagwa ophedwa m'dziko la Ababiloni, opyozedwa m'miseu yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adzavulazidwa ndi kufera m'dziko lonse ndi m'miseu ya mzinda wao womwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adzavulazidwa ndi kufera mʼdziko la Babuloni lomwelo ndi mʼmisewu yawo yomwe. |
Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati chovala cha ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira kumiyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.
Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m'miseu yake, ndipo anthu onse a nkhondo adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu.
Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m'miseu yake, ndi anthu ankhondo ake onse adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova.
Lupanga lili pa akavalo ao, ndi pa magaleta ao, ndi pa anthu onse osakanizidwa amene ali pakati pake, ndipo adzakhala ngati akazi; lupanga lili pa chuma chake, ndipo chidzalandidwa.
Ngakhale Babiloni adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yake, koma kuchokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.