Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.
Yeremiya 51:2 - Buku Lopatulika Ndipo ndidzatuma ku Babiloni alendo, amene adzampeta iye, amene adzataya zonse m'dziko lake, pakuti tsiku la chisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndidzatuma ku Babiloni alendo, amene adzampeta iye, amene adzataya zonse m'dziko lake, pakuti tsiku la chisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzatuma alendo ku Babiloni, kuti adzampepete ndi kuseseratu zonse zokhala m'dziko lake. Iwowo adzamuukira pa mbali zonse nthaŵi ya zoopsayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzatuma alendo ku Babuloni kudzamupeta ndi kuwononga dziko lake kotheratu. Iwo adzalimbana naye ku mbali zonse pa tsiku la masautso ake. |
Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele.
Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israele: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babiloni, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Ababiloni m'ngalawa za kukondwa kwao.
Ndawapeta ndi chopetera m'zipata za dziko; ndachotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao.
Memezani amauta amenyane ndi Babiloni, onse amene akoka uta; mummangire iye zithando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wake yense; mumbwezere iye monga mwa ntchito yake; monga mwa zonse wazichita, mumchitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israele.
Ndipo wonyadayo adzakhumudwa nadzagwa, ndipo palibe amene adzamuutsa iye; ndipo Ine ndidzayatsa moto m'mizinda yake, ndipo udzatentha onse akumzungulira iye.
Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.
chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.