mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?
Yeremiya 5:8 - Buku Lopatulika Anali onga akavalo okhuta mamawa; yense wakumemesera mkazi wa mnansi wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anali onga akavalo okhuta mamawa; yense wakumemesera mkazi wa mnansi wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aliyense ankathamangira mkazi wa mnzake, monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa, aliyense wa iwo ankathamangira mkazi wa mnzake. |
mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?
Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wa mwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.
Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?
Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.
chifukwa anachita zopusa mu Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.
Chifukwa mukondwa, chifukwa musekerera, inu amene mulanda cholowa changa, chifukwa muli onenepa monga ng'ombe yaikazi yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba;
Ha, ndikadakhala ndi chigono cha anthu aulendo m'chipululu; kuti ndisiye anthu anga, ndiwachokere, pakuti onse ali achigololo, msonkhano wa anthu achiwembu.
Ndipo wina anachita chonyansa ndi mkazi wa mnansi wake, winanso wadetsa mpongozi wake mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wake mwana wamkazi wa atate wake.
Usasirire mkazi wake wa mnzako; usakhumbe nyumba yake ya mnzako, munda wake, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.