Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?
Yeremiya 48:9 - Buku Lopatulika Patsani Mowabu mapiko, kuti athawe apulumuke; mizinda yake ikhale bwinja, lopanda wokhalamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Patsani Mowabu mapiko, kuti athawe apulumuke; midzi yake ikhale bwinja, lopanda wokhalamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mowabu mchenjezeni, chifukwa posachedwa asakazika. Mizinda yake isanduka mabwinja, ikhala yopanda anthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtsineni khutu Mowabu chifukwa adzasakazika; mizinda yake idzasanduka mabwinja, wopanda munthu wokhalamo. |
Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?
Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwa! Mwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu.
Pakuti ana aakazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka.
Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.
Mwana wamkazi iwe wokhala mu Ejipito, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsa, mulibenso wokhalamo.
Inu okhala mu Mowabu, siyani mizinda, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja chisanja chake pambali pakamwa pa dzenje.
Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.
Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a chiombankhanga chachikulu, kuti akaulukire kuchipululu, ku mbuto yake, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka.